×
Corrigir

Mpaka Udzipita

Langwan Piksy

Ndikudziwa kuti ndafika mammawa
Ndikudziwa zaku bhowa
Yeah mtima wako ukuwawa
Koma babe ukudziwa za ku bhawa

Ndimakupeza wagona
Sticheza ngati banja
Ine Ndimakhala ndatopa
Lonseli ndi vuto langa

Mammawa uliwonse ukumalira
Lero Ndakupeza ukupakila
Komano honey just hold on
I know I've done wrong
Komazi ndi zazing'ono
Nde

CHORUS
Mpaka udzipita
Sindufuna kusikidwa.
Zomwe ukufuna ine ndzichita ndikwanitsa

Yes I know I didn't give you much attention
Lately
Every time on the cellphone
Too much what'sapp, too much twitter
Umafuna kundikonda koma sinkupasa mita
Busy ntchito weekend ndi anzanga
Ndimalonjeza zinthu zochuluka simpanga
Umadandaula koma mmaiwala nsanga
Kuchitenga for granted chikondi chomwe umandipatsa
Mmalo molowera mmwamba I know we going down
Ndikale lomwe ndinayenda nawe mtown
Komano honey just hold on
I know I'm doing wrong
Komazi ndi zazing'ono
Nde

CHORUS
Mpaka udzipita
Sindufuna kusikidwa.
Zomwe ukufuna ine ndzichita ndikwanitsa

Usayese ndikutenga simple
Kwa ine utanthauza dziko
Chikondi chako chindipasa dzitho
Ndikamati ndine mphongo ndiwe

I swallow my pride ndameza matama
Ndameza zochuluka pa kamoz
Ndatsamwa
Ndiri ndi munda koma sinkupalira
Ndikudziwa sukukondwa mmomwe zikukhalira

Ndiwauza anzanga ino weekend
Sindioneka poti ndikhala ndiwe
Eh yah ndikhala ndiwe baby
Sindilora upite

CHORUS
Mpaka udzipita
Sindufuna kusikidwa.
Zomwe ukufuna ine ndzichita ndikwanitsa






Mais tocadas

Ouvir Langwan Piksy Ouvir